Zechariah 10

Yehova Adzasamalira Yuda

1Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira;
ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula.
Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu,
ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.
2Mafano amayankhula zachinyengo,
owombeza mawula amaona masomphenya abodza;
amafotokoza maloto onama,
amapereka chitonthozo chopandapake.
Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika
chifukwa chosowa mʼbusa.

3“Ine ndawakwiyira kwambiri abusa,
ndipo ndidzalanga atsogoleri;
pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira
nkhosa zake, nyumba ya Yuda,
ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.
4Mu Yuda mudzachokera mwala wapangodya,
mudzachokera chikhomo cha tenti,
mudzachokera uta wankhondo,
mudzachokera mtsogoleri aliyense.
5Onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo
zoponda mʼmatope a mʼmisewu nthawi yankhondo.
Chifukwa Yehova adzakhala nawo,
adzachita nkhondo ndi kugonjetsa okwera pa akavalo.

6“Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda
ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe.
Ndidzawabwezeretsa
chifukwa ndawamvera chisoni.
Adzakhala ngati kuti
sindinawakane,
chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo
ndipo ndidzawayankha.
7Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvu
adzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo.
Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala;
mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.
8Ndidzaliza mluzu
ndi kuwasonkhanitsa pamodzi.
Ndithu ndawawombola;
adzachulukana ngati poyamba paja.
9Ndinawamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu,
koma ku mayiko akutaliwo adzandikumbukira.
Iwo pamodzi ndi ana awo adzapulumuka,
ndipo adzabwerera.
10Ndidzawabweretsa kuchokera ku Igupto
ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya.
Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni,
mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.
11Adzawoloka nyanja ya masautso;
nyanja yokokoma idzagonja
ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa.
Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha
ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.
12Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehova
ndipo adzayenda mʼdzina lake,”
akutero Yehova.
Copyright information for NyaCCL